Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Ndondomeko ya mphamvu ku anthu yachiwiri akuikhazikitsa ku Lilongwe

Unduna woona maboma ang’ono ang’ono, umodzi komanso chikhalidwe mmawa uno ukukhazikitsa ndondomeko yachiwiri ya mphamvu ku anthu munzinda wa Lilongwe.

Mlozo wachiwiri-wu akonzamo zovuta zina zimene mlozo wakale  woyamba wa 1998 unali nawo zomwe  zimalepheretsa anthu kutukuka, kutenga mbali muzochitika zambiri zaboma komanso kuthandizidwa moyenera ndi makhonsolo osiyanasiyana a boma kuti mzika zikhale ndi mphamvu pochita zinthu.

Pamwambowu makhonsolo, adindo aboma, a  World Banki ndi ena  akhalanso ndi mwayi wophunzira momwe  ndondomeko yoyamba yathandizira dziko lino kudzera mu mloza wakalewo.

Nduna yoona maboma ang’ono, a Richard Chimwendo Banda, ndiwo akhazikitse mlozo wachiwiriwu.

Related posts

Use art against climate change — Chinsapo Arts Theatre

Romeo Umali

Mpikisano wa 1 NICO Netball watentha

Romeo Umali

CHIEFS CHALLENGED TO RECLAIM LEADERSHIP IN ECOSYSTEM RESTORATION

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.