Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Chitukuko chisaononge chilengedwe

Nduna yoona zamalo, a Deus Gumba, apempha anthu omwe amagwira ntchito yoyeza malo mdziko muno kuti atenge udindo oteteza zachilengedwe akamagwira ntchito zawo.

Ndunayi yanena izi ku Mangochi komwe yatsegulira msonkhano wapachaka wa masiku atatu wa anthu omwe anazama pazoyeza malo pansi pabungwe la Malawi Institute of Surveyors (MIS) komwe atsindika kuti anthuwa ali ndi udindo owonesetsa kuti zachilengedwe zikutetezeka mdziko muno.

“Chitukuko ndichabwino koma timaona kuti zitukuko zambili zimaononga chilengedwe kotelo anthuwa ali ndi udindo kuti akamavomeleza malo okuti pakhale zitukuko aonesetse kuti chilengedwe chisaonongeke,” anatero a Gumba.

President wabungweri Desmond Namangale wayamika boma chifukwa chowaika anthuwa patsogolo pokonza ma bilo atatu azamalo omwe nyumba ya Malamulo yawavomeleza.

Olemba: Davie Umar
#MBCDigital
#Manthu

Related posts

Alimi aguliretu mbewu zoyenera — SeedCo

MBC Online

Mudzafufuze abale anu — Zomba Mental

Romeo Umali

Bushiri apereka chimanga kwa mabanja 200 ku Mangochi

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.