Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Alimi aguliretu mbewu zoyenera — SeedCo

Kampani yopanga mbewu ya SeedCo yalangiza alimi kuti aguliretu mbewu zovomerezeka nyengo ya dzinja isanafike.

A Dennis Mdzalimbo, omwe amaona zamalonda  Ku kampaniyi  anati kugula mbewu zovomerezeka kumathandiza kuti ulimi ukhale waphindu.

Iwo amayankhula izi pa msonkhano omwe anachititsa ndi anthu komanso makampani omwe amagulitsa mbewu ochokera ku chigawo cha kumpoto.

A Mdzalimbo alangizanso alimi kuti adzitsatira ulangizi wa zanyengo kuti adzibzyala mbewu zogwirizana ndi momwe mvula ikugwera.

Malingana ndi akatswiri a zanyengo, madera ena m’chigawo cha kumpoto mugwa mvula yocheperako chaka chino kamba ka mphepo yotchedwa La Nina.

 

Olemba: Chimwemwe Milulu

Related posts

Chipatala cha Namatumi ku Thyolo achimaliza kumanga

Blessings Kanache

Malawi Parliament Chamber goes digital, installs e-Chamber system

Mayeso Chikhadzula

Tiyeni tiphunzirepo pa moyo wa Dr. Chilima – St Patrick’s Parish

Alinafe Mlamba
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.