Mneneri Shepherd Bushiri wagawa matumba a chimanga kwa mabanja okwana 200 amene anakhudzidwa ndi vuto lakusefukira kwa madzi m’dera la Mfumu yayikulu Nankumba ku Monkey-Bay m’boma la Mangochi.
Ngoziyi itadza, anthu ambiri anathawira ku malo ongoyembekezera otchedwa Nankhwali ndi Sungo.
A Aubrey Kusakala, amene amayankhulira a Bushiri, anati mneneriyu anali okhudzidwa koposa kotero, anaganiza zothandiza anthuwa.

Sub-Traditional Authority Chiwalo, nawo anathokoza a Bushiri kaamba ka zimenezi ndiponso anamema anthu ena akufuna kwabwino kuti achite zomwezi.
Aka ndi kachitatu kuti a Bushiri agawe chimanga m’bomali ndipo padakali pano, ntchito yogawa chimanga chaulere kwa anthu osowa yafikira anthu opyolera 700000 m’ma boma okwana khumi.
Olemba : Miriam Kaliza
#MBCDigital
#Manthu