Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

DR Usi apempha NEEF iganizire aphunzitsi

Wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, Dr Michael Usi, wapempha bungwe la NEEF kuti liganizire aphunzitsi aku pulaimale ndi ena akusekondale powatsekulira ngongole yawo yapadera yochitira bizinesi.

Dr Usi ati aphunzitsiwa amagwira ntchito yotamandika koma umoyo wawo umakakamira mu umphawi.

Iwo amaliza kuyendera anthu omwe apindula ndi ngongole za NEEF pa Chinkhoma Trading Centre ndipo akulunjika ku Bowe Farmers Cooperative m’boma lomweli la Kasungu.

“Ndikufuna kuti mukagula galimotozi mumangenso nyumba zokhalamo, awa nde maziko anu. Izi mwachitazi ndi zabwino ndithu,  koma pokhala mpofunikiranso,” atero a Usi.

Dr Usi anakwera imodzi mwa galimoto za anthu omwe apindula ndi ngongolezi nkuyendetsako.

Related posts

ROSAF URGES MOTORISTS TO  CONSIDER  VULNERABLE ROAD USERS

MBC Online

Police to deploy intelligence-driven operation

Romeo Umali

Two nabbed over K145.2 million robbery

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.