Unduna wa zamaphunziro mogwirizana ndi bungwe loona za mayeso la Malawi National Examinations Board (MANEB) ati mwa ophunzira a sitandade 8 okwana 252, 448 omwe analemba mayeso, ophunzira okwana 217,708 ndi omwe akhonza kuyimira 86.16% kusiyana ndi chiwerengero cha chakachatha cha 87.87% chomwe chinali chokwera.
Wapampando wa bungwe la MANEB a Dorothy Nampota ati ophunzira a fomu 2 okwana 163,950 omwe analembetsa, ophunzira 154,504 ndi omwe analemba mayesowa, ndipo 110,102 ndi omwe akhonza kuyimira 71.20% pomwe chaka chatha chiwerengero china 72.65%.
Nduna yazamaphunziro a Madalitso Kambauwa Wirima yayamikira bungwe la MANEB kamba kogwiritsa ntchito njira zamakono pantchito yawo yolembetsa mayeso komanso kutulutsa zotsatira za mayesowa munthawi yake.
A Kambauwa ati ophunzira omwe alemba mayeso akupulamaile a sitandade 8 ali ndikuthekera kowona ngati asankhidwa kapena ayi kudzera pa intaneti.