Kutsatira kuchuluka kwa imfa komanso ngozi zapamsewu zodza kaamba ka kabaza, bungwe lamadotolo owona za mafupa pamodzi ndi abwenzi osiyanasiyana akupitilira kufotokozera komanso kuphunzitsa anthu m’dziko muno malamulo komanso mmene angapewere ngozizi.
Bungweli lachititsa msonkhano ku Area 25 m’boma la Lilongwe lero, pomwe pali adindo osiyanasiyana ndipo akukambirana zokhudza chitetezo chapamsewu, maka muntchito za kabaza.
Malinga ndi bungweli, anthu 48 pa 100 aliwonse m’dziko muno amakhala ndi ulumali akachita ngozi yakabaza zomwe ati ndizodandaulitsa.
Wachiwiri kwa nduna ya zaumoyo, a Halima Daud, ati vuto langozi zakabaza likuchititsa kuti zipangizo zachipatala zidzichepa poti anthu ovulala akumakhala ochuluka.