Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Ndidzaimanso pa chisankho cha 2025’

Prezidenti wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, wati ndi wokonzeka kudzaimira chipani cha Malawi Congress MCP ngati msonkhano waukulu wachipani umene ukhalepo mmwezi wa August chaka chino utavomereza.

Dr Chakwera amayankhula pa msonkhano wachitukuko omwe anachititsa pa sukulu ya pulaimale ya Ndaula kwa Senior Chief Masumbankhunda mboma la Lilongwe.

“Ngati pali wina wokapikisana nane ali wokonzeka kutero, ine sindiopa mpikisano,” anatero  Dr Chakwera.

Pa misonkhano yosiyanasiyana, atsogoleri achipani cha MCP akhala akumalengeza kuti Dr Chakwera adzaimira chipanichi pa chisankho cha 2025 kamba ka masomphenya ake pa chitukuko.

Pamsonkhanowo,  Dr Chakwera anapemphanso mabungwe omenyera ufulu wa anthu mdziko  muno kuti adzionetsetsa kuti akuteteza ufulu wa anthu achikulire.

Pamenepa, mtsogoleri wadziko linoyu wapemphanso adindo onse m’dziko muno, kuphatizapo apolisi, kuonetsetsa akuti aliyense akutsata malamulo.

 

Olemba: Mayeso Chikhadzula

Print Friendly, PDF & Email

Author

  • Mayeso Chikhadzula joined MBC in 2006, he's an Investigative Journalist and Principal Reporter. He's also a News Anchor, Presenter, and producer.

Related posts

Govt geared to increase electricity access

MBC Online

MDF, MPS arrest 43 in Lilongwe security sweep

MBC Online

Super League rookies in overhaul

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.