Limodzi mwa mabungwe omwe si a boma lotchedwa M’badwa Zokhudzidwa lapempha zipani zonse zandale kuti zipereke ulemu oyenera kwa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, malemu Dr Saulos Chilima, ndikuonetsetsa kuti pasalowe ndale pankhani yamaliroyi.
M’neneri wa gululi, a Agape Khombe, wati akudziwa kuti pali zipani zina zomwe zikufuna kusokoneza mwambo oyika m’manda malemu Dr Chilima pofuna kuoneka abwino pa ndale.
Malemu Dr Chilima, omwe adamwalira pangozi ya ndege lolemba lapitali, ayikidwa m’manda Lolemba likudzali kwawo ku Nsipe ku Ntcheu.