Portia Kajanga, m’neneri wabungwe loona zamisewu
M’neneri wabungwe loona zamisewu mdziko muno la Roads Authority (RA), a Portia Kajanga, ati bungwe lawo latumiza makontalakitala m’misewu yonse ya m’dziko muno pofuna kukwilira maenje onse.
A Kajanga ati panali zinthu zina zimene zinachititsa kuti ntchitoyi ichedwerepo koma panopa zonse zili mmalo.
“Misewu ina siikufunika kukwilira mayenje koma kungokonzanso kawiri kukhala yatsopano ndipo wina ndi wa Chendawa omwe ukuyambira pa Kanengo mpaka ku Area 25 mu mzinda wa Lilongwe,” anatero a Kajanga.
Iwo ati msewu wa Area 49 kukafika pa Kaunda roundabout wokakumana ndi msewu wopita ku Mchinji aukonzanso kuti uzidutsa galimoto ziwiri mbali zonse.
Pa nkhani ya anthu omwe akumakwilira m’misewu nkumatenga ndalama kwa madalaivala, a Kajanga ati umenewu ndi mlandu kaamba kakuti bungwe lawo ndi lomwe lili ndi ukadaulo wokonza misewu ya m’dziko muno.