World Bank yapereka 80 million dollars (imene ndi pafupifupi K140 billion) ku boma la Malawi zothandizira pa ntchito zake zokweza chuma ndi miyoyo ya anthu m’dziko muno.
Kalata yomwe bankiyi yalembera nduna yazachuma, a Simplex Chithyola Banda, yati iyi singongole koma thandizo loti dziko la Malawi ligwiritse ntchito pa dongosolo lake lazachuma komanso kuonetsetsa kuti likupeza ndalama ndi zinthu zina zofunika kuti miyoyo ya anthu ipite patsogolo.
World Bank yati ndalamazi zithandizanso kuti boma lilimbikitse kalondolondo wa chuma chake, maka m’maunduna ndi nthambi zina za boma.
Sabata yatha, nayo banki ya mu Africa ya ADB inapereka ndalama zokwana 23 million dollars (yomwe ndi K40 billion) yothandiza pa dongosolo lazachuma cha dziko lino, patatha zaka pafupifupi khumi maiko ndi mabungwe akunja atasiya kuthandiza dziko lino.
Olemba: Blessings Kanache