Prezidenti wa chipani Cha PP, Dr Joyce Banda walengeza kuti chipanichi chidzakhala ndi msonkhano wake waukulu pa 7 September chaka chino mumzinda wa Lilongwe.
Iwo alengeza izi ku Nancholi komwe anachititsa msonkhano wandale.
Iwo ati ndi okondwa kuti chipani cha PP ndi champhamvu ku Blantyre ndipo apempha owatsatira kuti apitirize kusunga bata.
Khwimbi la anthu linasonkhana kumsonkhanowu pabwalo la Nancholi ndipo nawo aGeorge Nnesa, mtsogoleri wa chipani Cha Mafunde, analinso nawo pa msonkhanowu.
Olemba: Blessings Cheleuka
#MBCDigital
#Manthu