Chipani cha UTM chati ndipofunika kuti pakhale umodzi pakati pa anthu onse m’dziko muno pofuna kuti mwambo wokhuza wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino malemu Dr Saulos Chilima ndi anthu ena omwe anali nawo mu ndege yomwe inagwa lolemba mu nkhalango ya Chikangawa, uyende bwino.
Ofalitsankhani za chipanichi, A Felix Njawala anena izi pa msonkhano wa atolankhani omwe akuluakulu a chipanichi anachititsa ku Iikulu la chipanichi ku Area 10 mu mzinda wa Lilongwe.
Iwo apemphanso a Malawi kuti apewe mchitidwe wotumizirana zithunzi za ngoziyi kudzera mmasamba a mchezo.
Pa msonkhanowu panalinso mlembi wamkulu wa chipanichi, a Patricia Kaliati.
Thupi la malemu a Chilima likuyembekezeka kudzayikidwa m’manda Lolemba ku Nsipe m’boma la Ntcheu.