Mkulu wa kampani ya Airtel Malawi, Charles Kamoto, wati malemu Dr Saulos Chilima anali munthu wodzipereka ndi wokonda ntchito.
Poyankhula ndi MBC, a Kamoto ati kampani ya Airtel Malawi sidzaiwala zazikulu zomwe adachita posintha kagwilidwe ka ntchito kumpaniyi.
“Ma tower ambiri omwe mukuwaona m’dziko muno a Airtel, malemu a Chilima ndi omwe adathandizira kuti ayike malo osiyanasiyana,” anatero a Kamoto.
Iwo anati adaphunzira zinthu zambiri kuchokera kwa malemu Dr Chilima.
Malemu Dr Chilima adagwilako ntchito ku kampani zosiyanasiyana m’dziko muno, kuphatizapo Airtel Malawi, asadayambe kuchita za ndale.