Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Unduna oona za madzi wati upitilira kupereka madzi abwino

Anthu oposa 146,000 a m’maboma a  Ntcheu ndi Balaka akuyembekezeka kukhala ndi madzi abwino komanso aukhondo kudzera ku ntchito yopopa madzi mu nthaka pogwiritsa ntchito  mphamvu ya dzuwa, pansi pa ndondomeko  ya Mpira-Balaka Water Supply System.

Izi zadziwika pamene wachiwiri kwa nduna yoona za madzi, a Liana Kakhobwe Chapota, anayendera malo opopa madziwa a  Njereza komanso Bawi m’bomali.

Malinga ndi undunawu, pakadalipano boma layika mipopi yoposa  1600  m’boma la Ntcheu ndipo mwa mipopiyi, 1214 yayamba kale kugwira ntchito.

A Chapota  ati boma likufunitsitsa kuti pofika 2030, aMalawi ochuluka athe kupeza madzi abwino komanso aukhondo mosavuta.

Pakadalipano, mkulu wa za madzi ku Ntcheu, a Onanses Nyirenda, ati apeza ndalama zoti zithandizire kugula ma paipi oonjezera kuti athe kupereka madzi abwino wa  kwa anthu ochuluka m’bomali.

Bungwe la World Bank, mogwirizana ndi boma, linaika ndalama zoposa K140 billion  kuti zithandizire anthu ku ngozi zogwa mwa dzidzidzi ndipo mwa ndalamazi, K1.4 billion anaipatula kuti amangire Mpira – Balaka water supply system.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Ng’oma mourned

Olive Phiri

GOVERNMENT MOVES ON SALIMA SUGAR COMPANY

McDonald Chiwayula

COURT THROWS OUT FORMER ANGLICAN BISHOP MALASA INTERLOCUTORY INJUNCTION

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.