Mwini wake wa kampani imene imagulitsa zipangizo zophodera za amayi ya the Nail Room, Atupele Chindevu, wati adzithandiza ligi ya chigawo chapakati yampira wamanja popereka mphotho kwa amene adzichita bwino kwambiri pamasewero kuposa wina aliyense.
A Chindevu ati ayika padera ndalama yokwana K1 million ndipo adzipereka K50,000 kwa osewera yemwe adzichita bwino kuposa anzake onse pasabata.
“Ndikufuna kuti atsikana akhale ndi chidwi pamasewero awo. Timanva kukoma kwambiri timu yathu yadziko ya Queens ikamapambana ndipo kuti idzichitabe bwino tikuyenera kupereka chikoka ku ma ligi ang’onoang’ono,” anatero a Chindevu.
Poyankhula atasayinirana mgwirizano, wapampando wa Central Region Netball League, a Fernando Ligora, ati ndiokondwa kwambiri kaamba ka thandizoli ndipo ati achita chilichonse chothekera kuti mgwirizanowu upindulire mbali zonse ziwiri.