Bishop Mthandizi Suzgo Nyirenda wa Diocese ya Mzuzu mu mpingo wa Katolika wapempha aMalawi kuti alilire Mulungu ndi cholinga choti dziko lino lilandire mayankho pa zovuta zosiyanasiyana.
Iwo anatinso kutsogoza pemphero mu zinthu zonse kuphatikizapo kupemphelera atsogoleri ndi za mtengo wapatali.
Bishop Nyirenda amayankhula izi pa mwambo wa misa yomwe imachitikira pa mpingo wa Katolika wa St. Peters mu mzinda wa Mzuzu.
Iwo anati atsogoleri ali ngati chotengera, koma mwini wake opereka zosowa za anthu ndi Mulungu.
Potsindika pa nkhaniyi Bishop Nyirenda analalikira pa mau ochokera m’buku la Eksodo mutu 16 pomwe pali nkhani ya Mose yemwe Mulungu anamugwiritsa ntchito kuti atsogolele ana a Israeli.
Olemba: Jackson Sichali