Mkulu wa Chimbota Community Development Organisation m’boma la Nkhatabay a Kevin Troughton wati posachedwapa bungweli limanga chipatala ku Bwelero mdera la Sub – TA Ndola m’bomali.
Troughton walankhula izi lero mderali pomwe bungwe lake limapereka holo yomwe amanga ya ndalama zokwana K70 million pa Chimbota Private Secondary School m’bomali.
“Lero tapereka holo-yi yomwe ithandize pa ntchito zosiyanasiyana monga ophunzira kulemberamo mayeso, misonkhano ya sukulu komanso zikondwelero monga zaukwati mwa zina,” watero Troughton.
Iye waonjezela kunena kuti aonetsetsa kuti amanganso chipatala mderali kaamba koti zipatala zili motalikilana ndipo anthu amavutika mayendedwe chifukwa cha miseu komanso mapiri.
Mlendo olemekezeka pa mwambowu a Grace Kwelepeta ayamikira bungweli pogwira ntchito zachitukuko zomwe akuti zithandiza kulimbikitsa maphunziro ndi zina.
Mmau ake Sub – TA Ndola wadzudzula mchitidwe wa anthu ena omwe amakaniza alendo kupeza malo mmbali mwa nyanja komanso kumudzi ponena kuti mchitidwewu uli ndikuthekera kotsekereza ntchito za chitukuko zomwe zingathandize anthu ambiri.
Bungwe la Chimbota Community Development lamanga holo-yi ndi ndalama zochokera ku Beit Trust ndipo likugwira ntchito zake mmaiko a Zambia, Zimbabwe ndi Malawi komwe akulimbikitsa ntchito zaumoyo komanso maphunziro.
Olemba George Mkandawire.