Msonkhano wa akuluakulu a m’maboma mchigawo chakumpoto uli mkati komwe nkhani yaikulu ndi ya chitetezo panthawi ya chisankho, chomwe chichitike chaka chamawa.
Poyankhula pamene amatsekulira msonkhanowu, mmodzi wa makomishonala abungwe loyendetsa chisankho m’dziko muno la MEC, a Anthony Mukumbwa, ati chisankho sichingayende bwino ngati palibe chitetezo chokwanira.
Iwo ati ichi ndi chifukwa chake malamulo atsopano achisankho ayika udindo waukulu wa chitetezo kwa akuluakulu apolisi am’maboma.
“Tikukumana ndi ma DC am’maboma komanso akuluakulu apolisi ndicholinga chakuti adziwe udindo omwe ali nawo pankhani zachitetezo ndi zina, malinga ndi malamulo atsopano oyendetsera chisankho,” a Mukumbwa anafotokoza.
Kumsonkhanowu kuli ma DC amaboma onse achigawo chakumpoto komanso akuluakulu a polisi mchigawochi.
Wolemba: Henry Haukeya