Wapampando wa komiti yomwe yakonza msonkhano waukulu wa chipani cha Malawi Congress a Kezzie Msukwa walangiza mamembala a chipanichi kuti apitirize kukhala pambuyo pa Prezidenti Dr Lazarus Chakwera, yemwenso ndi mtsogoleri wa chipanichi.
A Msukwa alangizanso mamembala a chipanichi kuti apitirize kusunga mwambo mchipani komanso kumvera mtsogoleri wa chipanichi.
Iwo ati ali ndi chikhulupiliro kuti chipani cha MCP chidzapambana pa chisankho cha chaka chamawa.
Olemba: Isaac Jali ndi Olive Phiri