Apolisi munzinda wa Lilongwe amanga a Tsisa Mbangali azaka 26, powaganizira kuti anagwililira mlamu wawo wazaka 13 ndi kumupha.
Ofalitsankhani za polisi ya Lilongwe, a Hastings Chigalu, ati izi zachitika ku Area 36 munzindawu, kumene a Mbangali amakhala ndi banja lawo komanso mwanayo, amene ndi mng’ono wa mkazi wake.
A Chigalu ati pakati pa usiku wa pa 25 January, mwamunayo anadzutsa mkazi wake kuti mnyumbamo mwalowa munthu wachilendo koma atadzuka, sanapeze munthu aliyense.
Kenako banjalo litayang’ana pamene mtsikanayo amagona, sanamupezepo. Ndipo atatuluka panja, anapeza mwanayo ali m’munda wa chimanga koma atafa.
Kafukufuku wa apolisi anasonyeza kuti a Mbangali ndiwo adachita izi komanso zotsatira za chipatala zidasonyeza kuti mtsikanayo adafa chifukwa wina anamumenya m’mutu ndi chitsulo.
Mbangali amachokera m’mudzi wa Buluzi kwa mfumu yayikulu Kalumba m’boma la Lilongwe.