Mmodzi wa akuluakulu a kampani zopanga bread za Nyanja Bakery, Olympic Bakery komanso BreadTalk, Saizi Bakali wati ndiokonzeka kutsitsa mtengo wa bread mokomera a Malawi ngati kampani zopanga ufa wa tiligu zingatsitse mtengo ogulira ufawu.
Bakali wanena izi pamene akulukulu akampani zosiyanasiyana akukumana ndi nduna yaza malonda ndi mafakitale, a Sosten Gwengwe komanso mkulu wa banki yayikulu m’dziko, a MacDonald Mafuta Mwale komwe akukambirana zotsitsa mitengo ya katundu osiyanasiyana.
Mkulu wa kampani yopanga ufa ya Bakhresa, a Rao Pattipati Bakhresa wati ndiwokhutira ndi zokambirana zomwe zachitika lachitatu ndi a Gwengwe ndi a Mwale.
A Bakhresa ati a Malawi ayembekezere kuti pofika sabata ya mawa anthu awona kusintha kwakukulu pa msika.
Iwo ati malinga ndi zomwe a Reserve Bank awatsimikizira, zinthu ziyenda bwino posachedwapa.
Ena mwa omwe akukumana nawo nkuphatikizapo opanga bread ndi ufa wa bread, kampani zogulitsa nkhuku ndi zakudya za nkhuku, kampani yopanga mafuta wophikira komanso kamapani zopanga sopo.