Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Tithandizeni kuthana ndi ngongole – Mzuzu City Council

Khonsolo ya mnzinda wa Mzuzu yapempha komiti yakunyumba yamalamulo yoona momwe chuma chaboma chikugwilira ntchito ya Public Accounts Committee kuti ithandizirepo pamavuto angapo omwe khonsoloyi ikukumana nawo.

Pempholi laperekedwa pomwe komitiyi inayendera khonsolo ya Mzuzu pofuna kumva momwe ikugwilira ntchito zake komanso momwe ntchito zachitukuko zikuyendera.

“Tikukumana ndi zovuta monga ngongole yokwana K2 billion yomwe tikupempha boma lilowelerepo, kuyima kwa ntchito zachitukuko chifukwa chakuyima kwa ndalama zantchitoyi, kuchuluka kwa chiwerengero cha anthu ogwira ntchito mwamavuto ena,” mkulu wa khonsoloyi, a Gomezgani Nyasulu, anatero.

Mkulu wa Mzuzu City Council, Gomezgani Nyasulu, kufotokoza.

Poyankhapo pankhanizi, wapampando wa komitiyi, a Mark Botomani anati amva zamavutowa ndikuti nawo atula nkhawazi kuboma ndikufufuza zomwe zikuchitika pofuna kuonetsetsa kuti mavuto omwe akuyimitsa ntchito zachitukuko.

A Botomani anati komitiyi ndiyosangalala ndi ntchito zomwe awona zomwe anati zikugwirizana ndi masomphenya achitukuko cha Malawi 2063.

“Koma pankhani za ndalamazi pali zambiri zomwe khonsoloyi ikuyenera kuchita pothana ndi zinthu monga ngongole yomwe ali nayo,” anatero a Botomani.

 

Olemba: Henry Haukeya

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Old Mutual equips journalists on New Pensions Act

Earlene Chimoyo

Bandera ali mchitokosi pomuganizira kuti anazembetsa mtsikana wachichepere

Davie Umar

GAS DISTRIBUTORS URGED TO BROADEN SALES

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.