Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Wobera anthu m’magalimoto amugamula zaka zitatu kundende

Bwalo la milandu la First Grade Magistrate ku Karonga lagamula a Mussa Banda kuti akakhale kundende kwazaka zitatu ndikugwira ntchito yakalavula gaga chifukwa chopezeka olakwa pamilandu iwiri yobera anthu mumagalimoto.

Bwaloli, kudzera kwa oyimira boma pamilandu, a George Manda linamva kuti a Banda pa 10 August chaka chino, ananyamula a Keshton Matandala mugalimoto yawo ya Honda Fit pa Tobi m’msewu wa M1 pomwe amapita ku Rumphi kukagula mtedza.

Patangodutsa nthawi pang’ono, galimotoyo inayima ndipo oyendetsa anati sapitilira ndi ulendowu.

Atamva izi, a Mwatandala anafuna kutsika ndipo anayesetsa kutsegula chitseko koma anaona kuti chinali chotseka.

Kenaka bwaloli linamva kuti m’modzi mwa anthu amene anali nawo mugalimoto  anayesa kuwathandizira kutsegula chitseko ndipo zinatheka.

Atatsika, a Matandala anazindikira kuti ndalama zawo zokwana K1.7 million zikusowa muchikwama chawo.

Malinga ndi a Banda pofotokezera bwaloli, izi zinachitikiranso a Kondwani Mwanganda omwe anaberedwanso K2 million pa 11 August 2024 pomwe amapita ku Rumphi  kukagulanso mteza.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mutharika wati aMalawi adzilima mbewu zopilira ng’amba

Charles Pensulo

CFTC to probe sugar price hike

Earlene Chimoyo

Man drowns in Dwambadzi River

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.