Malawi Broadcasting Corporation
Agriculture Local Local News Nkhani

Alimi asamale pogula mbewu — Self Help Africa

Bungwe la Self Help Africa lalangiza alimi m’boma la Dedza kuti asamale pogula mbewu ndi zipangizo za ulimi mu nyengo ya dzinja chifukwa akagula mbewu zachinyengo zimabwezeretsa ulimi pambuyo.

M’modzi wa akuluakulu ku bungweli, a Ruben Kainga, amayankhula izi Lachitatu m’bomali pa chionetsero cha mbewu ndi zipangizo za ulimi zosiyanasiyana.

Chionetserochi chinachitika pamisika ya Chimbiya, Lobi, Bembeke komanso Dedza Boma.

A Kainga anauzanso alimi kuti kugula mbewu kwa ogulitsa ovomerezeka zikhoza kuwathandiza kuti adzapeze phindu paulimi wawo.

Mlangizi wamkulu woyang’anira ulimi ku Lobi EPA, a Madalitso Machira, anati chigawo chawo chili ndi mabanja alimi okwana 27,082 amene akuyembekezeka kugula mbewu ku kampani zovomerezeka.

A Machira anayamikiranso mabungwe a Self Help Africa komanso Kadale Consultants chifukwa chowathandiza alimi kuti agule mbewu mosavuta komanso pamtengo osaboola m’thumba.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

‘Masewero opalasa njinga ali ndi tsogolo’

MBC Online

Phase three to cover eight councils- MEC

MBC Online

We are a people who love and respect one another — Chakwera

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.