Olemba: Timothy Kateta
Zokonzekera za mwambo wa misa yapadera yokumbukira yemwe adali wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, malemu Dr Saulos Chilima, zili mkati ku Nsipe m’boma la Ntcheu.
Mapempherowa akuyembekezeka kuchitika loweruka lino pa 20 July.
Mwambo wa Misayi uchitika patatha masiku 40 chichitikireni ngozi ya Ndege imene idapha malemu Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu mu nkhalango ya Chikangawa pa 10 June chaka chino.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Michael Usi, akuyembekezeka kukakhala nawo pamwambo wamapempherowu, umene udzachitikire pa bwalo la Nsipe Catholic, pafupi ndi manda amene kudaikidwa malemu Chilima.
Enanso womwe akuyembekezeka kudzakhala nawo ku mwambowu ndi Inkosi ya Makhosi Gomani yachisanu, akuluakulu aboma ndi mafumu.
Bishop Peter Adrian Chifukwa wa Dedza Diocese ndi yemwe adzatsogolere mapempherowa.