Bank ya NBS yathandiza anthu okalamba komanso a ulumali ndi matumba a ufa wa chimanga kummwera kwa boma la Chiradzulu.
Poyankhula popereka thandizoli, mkulu wa Branch ya Limbe, a Twaibu Nnani, ati bankiyi ipitiriza kuthandiza osowa kudzera mu njira zosiyanasiyana.
Ndipo mfumu yaikulu Mpunga yapempha mabungwe akufuna kwabwino kuti athandize mabanja omwe akhudzidwa ndi njala.
Malinga ndi a Mpunga thandizoli ati ndi lapafupifupi K3.5 million.
Wolemba: Blessings Cheleuka