Mkulu wa mabwalo a milandu m’dziko muno, Justice Rizine Mzikamanda, walangiza oweruza milandu mumabwalo osiyanasiyana kuti adzilemekeza malumbiro awo pogwira ntchito yawo mwachilungamo.
A Mzikamanda anena izi pomwe amalumbilitsa oweruza milandu atsopano asanu ndi anayi omwe amaliza maphunziro awo apadera a miyezi 6 atagwira ntchito yoimira anthu pamilandu kumabungwe osiyanasiyana.
A Mzikamanda ati mdziko muno anthu ambiri akusakasaka chilungamo chomwe nthawi zambiri chimabwera mochedwa kapenanso kukhotetsedwa kumene kamba kakuchepa kwa oweruza pena kusakhulupirika pantchito kwa oweruza milandu omwe alipo kale.
M’mawu ake, m’modzi wa oweruza milandu omwe angolumbiritsidwa kumenewa, a Ramai Muhamad, anati ayesetsa kugwira ntchito mokhulupirika potsatira malamulo.
Oweluza milandu atsopanowa awatumiza m’maboma osiyanasiyana kuti athandizire pa lingaliro lofuna kukhala ndi ma Senior Resident Magistrate m’boma lilolonse m’dziko muno.