Malawi Broadcasting Corporation
Local

Tifikira a Malawi  onse omwe akuvutika ndi njala

Mtsogoleri wa mpingo wa Enlightened Christian Gathering, The Jesus Nation, Mneneri Shepherd Bushiri wapempha andale ndi amipingo kuti ayambe ayiwala zakusiyana kwawo pandale ndi zikhulupiliro ndikuyamba kuthandiza a Malawi omwe akhudzidwa ndi njala maaka mmadera omwe kunagwa ngozi zogwa mwadzidzi.

A Bushiri alankhula izi  kwa Mkando m’boma la Mulanje pomwe akupitiliza ntchito yogawa chimanga cha ulere kwa a Malawi ovutika ndi njala

Mneneri Bushiri pomwe amagawa chimanga m’chigawo cha kummwera

Iwo  ati ino sinthawi yolimbana pa ndale kapena zikhulupiliro koma yogwirana manja populumutsa miyoyo ya a Malawi omwe akusowa chakudya mmadera osiyanasiyana

“Chakudyachi ndikugawa kulikonse posaona kuti awa amatsatira chipani chanji kapena amapemphera mpingo uti, onse ovutika ndi njalawa ndi a Malawi,” atero a  Bushiri.

Ntchitoyi tsopano yapindulira anthu am’maboma a Thyolo, Mulanje, Ntcheu komanso Lilongwe. Malinga ndi a Bushiri  anthu pafupi-fupi 50,000 ndi omwe alandira thandizoli.

Pali chiyembekezo choti  maboma enanso mdziko muno alandira  thandizoli masiku akudzawa.

#mbconlineservices

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Save the Children hands over assets to partners

Paul Mlowoka

Boma la Neno lichita bwino polimbana ndi Edzi

MBC Online

POLICE RESCUE TWO FROM MOB

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.