Malawi Broadcasting Corporation
Health Local Local News Nkhani

Malawi ipindula ndi ntchito yotukula luso lazaumoyo

Boma la United Kingdom, kudzera ku bungwe la Global Health Partnerships, lakhazikitsa ntchito yothandizo kutukula luso la anthu ogwira ntchito zaumoyo m’dziko muno.

Mlembi wamkulu mu unduna wa zaumoyo, Dr Samson Mndolo, wati kudzera muntchitoyi, sukulu ya Kamuzu University of Health Sciences pamodzi ndi mabungwe a Medical Council of Malawi komanso Nurses and Midwives Council of Malawi alandira ndalama zokwana pafupipafupi K2.6 billion zogwilira ntchitoyi.

Cholinga chake ndi kuti anthuwo akhale ndi ukadaulo komanso kuonjezera luso lamomwe angasamalire odwala komanso momwe angathanirane ndi matenda osiyanasiyana.

M’modzi mwa akuluakulu ku ofesi yakazembe wa dziko la Britain m’dziko lino, a Dan Pine, ati ogwira ntchito zaumoyo m’dziko muno akhala akusowekera ukadaulo wamaphunziro a mmene angagwilire ntchito zawo.

A Pine ati uwu ndi mwayi waukulu kuti mayiko opindula kuthandizoli apititse ntchito za umoyo patsogolo kuyambira mwezi uno mpakana wa January chaka cha mawa.

Dziko la Malawi ndi limodzi mwa mayiko atatu oonjezera omwe apindule ndi ntchito yothandizira kutukula luso la anthu ogwira ntchito zaumoyo.

Maiko a Ghana, Nigeria komanso Kenya ndi amene anali oyambilira kupindula ndi ntchitoyi.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

MADONNA JETS IN

MBC Online

CHOLERA OUTBREAK IN MULANJE

Mayeso Chikhadzula

Trump escapes assassination attempt

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.