Apolisi ku Limbe mu mzinda wa Blantyre ati akufufuzabe chifukwa chimene John Mwanamvekha, wazaka 26, wadziwombelera ndi mfuti.
Ofalitsankhani wapolisi ku Limbe, Aubrey Singanyama, wati izi zachitika loweruka ku Chigumula ku Blantyre.
Malinga ndi a Singanyama, John anadzitsekera mu galimoto asanadziombere.
Malemuyo anali wa m’mudzi wa Namathiya, mfumu yaikulu Mpunga m’boma la Chiradzulu.