Bishop William Mchombo wa mpingo wa Anglican mu diocese ya Uppershire walimbikitsa a khristu kuti akhale oyanjana ndi odzipereka pofuna kupititsa patsogolo ntchito ya utumiki.
A Mchombo amayankhula izi m’boma la Mangochi pamene amatsogolera mwambo wa Misa yoyera pa mpingo wa Saint Andrews Anglican Church (Mangochi Parish).
Iwo ati ndi udindo wa akhristu kutenga gawo polimbikitsa umodzi komanso kulolerana mu zonse posatengera kusemphana maganizo komwe kwakhala ku kuchitika zaka zam’mbuyomu.
Bishop William Mchombo analimbikitsanso a Khristu a mpingowu kuti akhale ndi chidwi chotenga nawo mbali pantchito zina zachitukuko, monga kusamala ndi kuteteza chilengedwe pofuna kuchepetsa mavuto odza kaamba ka kusintha kwa nyengo.
Olemba: Owen Mavula