Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Thupi la Malemu Hope Chisanu lafika m’dziko muno

Thupi la yemwe anali ochita zisudzo komanso muulutsi, malemu Hope Chisanu, lafika m’dziko muno kudzera pa bwalo la ndege la Kamuzu International Airport munzinda wa Lilongwe kuchokera ku dziko la America. 

Nduna za boma, akatswiri owulutsa mau pa wayilesi, azisudzo, oyimba ndi ena ambiri ndi omwe anasonkhana kukalandira malemuwa.

Thupi la malemu Hope Chisanu alitengera ku Nthunzi Funeral Home ndipo mawa litengedwa kupita kumwambo wa mapemphero ku mpingo wa PCM ndipo kenako adzalinyamula kupita nalo kwa Kamphata, kumudzi kwawo, komwe lidzayikidwe mmanda lachinayi.

 

Wolemba: Yamikani Makanga

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mangochi Police drill Kabaza operators on road safety

MBC Online

Ntchito yopanga ziphaso ku Mangochi ikutheka

Chisomo Break

PRISAM TO LAUNCH SACCO FOR PRIVATE SCHOOLS

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.