Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Tabitha Chawinga tsopano ndiwa Lyon

Katswiri omwetsa zigoli wa timu yampira wa miyendo ya amayi, Tabitha Chawinga, akhale akusewelera timu ya Lyon ya mdziko la France pomwe wachita mgwirizano wa zaka zitatu ndi timuyi.

Chawinga, yemwe amasewera pa ngongole Ku timu ya PSG ku France komweko, anaonetsa ukadaulo pomwe adapambana mphotho ya omwetsa zigoli zambiri komanso adasankhidwa ngati katswiri yemwe adasewera bwino kwambiri kuposa onse mu ligi ya atsikana ya m’dziko la France mu season yathayi.

Kupita kwa Tabitha Ku Lyon tsopano ndichiyambi cha moyo wina pomwe tsopano wachokeratu ku timu yomwe wakhala alinayo mgwirizano m’dziko la China ya Wuhan Jiangda.

Related posts

Nzika ya Niger akuyisunga ku Maula

Romeo Umali

Gogo Chatinkha Maternity Ward wears a new face

MBC Online

Bungwe la CHEFO lichilimika kusunga khalidwe

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.