Achinyamata makumi atatu lero akuyembekezera kupata mwayi wa mpamba oyambira malonda okwana K1 million aliyense kuchokera kwa mayi Triephornia Mpinganjira ku BICC mu mzinda wa Lilongwe.
Izi zili pansi pa ndondomeko yomwe adakhazikitsa yothandiza achinyamatawa yotchedwa Kuthandiza Omwe Alibe Kuthekera Kupita Patsogolo.
Zokonzekera mwambowu zili m’chimake ndipo mayi Mpinganjira komanso Dr Thomson Mpinganjira ndi amene atsogolere mwambowu.
Pachiyambi, mayi Mpinganjira adayika ndalama zokwana K18 million pofuna kuthandiza achinyamata 18 koma chiwerengerochi chidakwera kufika pa achinyamata 34 pomwe nawo Dr Thomson Mpinganjira adaonjezera K14 million pomwe kampani ya Credible Investments Limited idathandizanso ndondomekoyi ndi K2 million.
Akuluakulu ena ochita malonda monga Dr Napoleon Dzombe komanso mkulu wa kampani ya Imosys, a Mayamiko Nkoloma akuyembekezeka kukhalanawo ndi kuyankhula ndi achinyamatawa pamwambowu
Mayi Triephornia Mpinganjira adakhazikitsa ndondomekoyi pa 16 April chaka chino ndipo achinyamata anayi oyamba adalandira kale mpambawu.