Malawi Broadcasting Corporation
Business Development Local Local News

Standard Bank yapanga phindu lokwana K52.5 billion mu 2023

Banki ya Standard yapanga phindu lokwana K52.5 billion, boma litadulapo kale msonkho, chaka chatha.

Phinduli ndilokwera ndi 34 percent poyerekeza ndi phindu lokwana K39.2 billion lomwe bankiyi inapanga mu chaka cha 2022.

Poyankhula pa msonkhano wa pa makina a internet wa anthu amene anayika ndalama zawo mu bankiyi, mkulu wa Standard Bank, a Phillip Madinga, ati phinduli alipeza kamba koti ndalama zomwe apanga chaka chatha zakwera kamba koti, mwazina, ndalama zomwe anthu amasungitsa ku bankiyi zinakwera.

A Madinga awonjezera kuti ayika njira zoyenelera kuti phinduli lipitilire kukwera chaka chino.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

LL Police recovers stolen TV, nabs suspect

Romeo Umali

COURT ADJOURNS AKSTER’S ARMS POSSESSION CASE

MBC Online

HRCC salutes Kasambara’s legacy

Blessings Kanache
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.