Banki yayikulu m’dziko muno ya Reserve yati lamulo ligwira ntchito kwa anthu onse amene akugulitsa, kugula ndi kuononga ndalama za chitsulo.
Mu chikalata chomwe wasayinira ndi Gavanala wa bankiyi, a Wilson Banda, bankiyi yati olakwa adzilipira chindapusa chokwana K5 million.
M’sabata zapitazi, anthu ambiri akhala akutsatsa ndalama zachitsulo monga K5 ndi K10 ndipo zadziwika kuti anthuwa amasungunula ndi kuphwanya ndalamazi.