Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Chakwera adzipereka pochepetsa vuto la nyumba

President Dr Lazarus Chakwera wati boma likudziwa kuti m’dziko muno muli vuto losowa nyumba.

Koma iye wati boma lake layambapo ntchito yotchedwa – Project 250. Kudzera muntchito-yi boma limanga nyumba zolimba zopilira ku mavuto ogwa mwadzidzidzi.

“Lero ndine okondwa kuyambitsa project yotchedwa Project 250, pomwe timange nyumba 250,000  zatsopano ndipo nyumba 500 zamangidwa kale,” anatero Dr Chakwera.

Iye anati m’mbuyomu chaka ndi chaka aMalawi amanamizidwa kuti amangiridwa nyumba, ena mpaka kunamizidwa kuti apatsidwa malata koma nyumbazo sizinamangidwe.

Mtsogoleri wa dziko linoyu anati masomphenyawo anali abwino koma akuluakulu ena amazikundikila okha, m’malo moti ntchitoyo ipindulire aMalawi.

Iye anayamika Dr Joyce Banda kaamba koyesetsa kumangilmra anthu nyumba pa zaka ziwiri zomwe analamulira dziko lino.

“Wina asakunamizeni, vuto lakuperewera nyumba ndi lalikulu zedi, ndipo titaliunikila, tinaona kuti tiyambile pa asilikali azachitetezo, chifukwa tonse sitingagone mwa mtendere, asilikali athu alibe pokhala,” anatero Dr Chakwera.

Mtsogoleri wa dziko linoyu anati anayambira pa nyumba 10,000 za asilikaliwa  zomwe zikumangidwa mdziko muno.

Dr Lazarus Chakwera anati mwa nyumba 10,000, nyumba 1,000 zatha kale.

A Chakwera anatinso pomaliza kuwatumikila a Malawi mchaka cha 2030, chiwerengero cha nyumbazi chidzaposa  10,000.

Iye anathokozanso President wakale  Dr Bakili Muluzi komanso Dr Joyce Banda chifukwa chodzipereka kumangira anthu nyumba, pamene dziko lino linakhudzidwa ndi Namondwe Freddy.

Mtsogoleriyu wati makampani ndi mabungwe ena ndi okonzeka kuthandiza pa ntchito yomanga nyumba kuphatikizapo kampani ya Henan Housing yaku China.

Cholinga cha msonkhano wa  National Housing Symposium ndikufuna kupeza njira zochepetsera vuto lakupelewera kwa nyumba mdziko muno, komanso kulimbikitsa anthu kumanga nyumba zamphamvu zopilira ku ngozi zogwa mwadzidzidzi.

Pa mwambowu, unduna wa zamalo awonetsa mapulani a nyumba zatsopano zomwe anthu azimanga kumudzi kuti pofika 2063, midzi idzaoneke ngati tauni.

 

Olemba Isaac Jali

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Sheriffs seize Bullets’ bus over K25 million debt

MBC Online

Two win big in TNM’s Tikolore Promotion

Chisomo Break

Young Stunna wafafaniza machimo ku Blantyre

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.