Khonsolo ya mnzinda wa Lilongwe yati sizoona kuti ogwira ntchito ku khonsoloyi amagawana katundu yemwe alanda kwa anthu ogulitsa malonda m’malo osayenera.
Mfumu yamnzinda wa Lilongwe, a Richard Banda, alankhula izi pomwe bungwe la Citizen Alliance linachita msonkhano ndi khonsoloyi okambirana zomwe khonsoloyi ikuchita pamavuto ena amunzindawu, omwe bungweli linanena kuti achitepo kanthu.
Malinga ndi a Banda, katundu yemwe amalanda kwa anthu ogulitsa malonda mmalo osayenera amamusunga ndipo amadzamugulitsa pa okushoni.
Pakadali pano, mtsogoleri wa Citizen Alliance, a Baxton Nkhoma, wati ndiokhutira kuti khonsoloyi ikuyesetsa kuthana ndi ena mwa mavuto omwe anawauza kuti achitepo kanthu.