Nthambi yoona za nyengo yati namondwe Chido tsopano wabwelera m’dziko la Mozambique atachepa mphamvu.
Mkulu oona za nyengo ku nthambiyi, a Lucy Mtilatila, ati namondweyu watuluka asanaononge kwambiri monga momwe amaonekera.
Iwo ayamikira anthu m’dziko muno chifukwa chosatira mwachidwi mauthenga ochenjeza omwe nthambiyi komanso nthambi zina zimapereka othandiza kuteteza miyoyo komanso katundu.
A Mtilatila ayamikiranso nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya DoDMA yomwe imathandizira kupereka mauthenga ochenjeza kudzera pa lamya za mmanja.
Pamenepa, a Mtilatila ati a Malawi akhale omasuka kaamba koti palibenso chiopsezo chilichonse cha namondweyu.
Olemba: Charles Pensulo