Wapampando wamwambo wa MBC Zokonda Amayi wa chaka chino, mayi Mervis Senga, ati zonse zokonzekera zamwambo wa Zokonda Amayi Macheza umene uchitikire munzinda wa Mzuzu zili mchimake.
Mayi wafuko lino, Madam Monica Chakwera, ndi amene akuyembekezeka kukhala mlendo olemekezeka pamwambowo.
A Senga ati padakali pano amayi oposa 400 kuchoka muzigawo zonse zadziko lino ndiamene afika kale kudzakhala nawo kumwambo okondwelera tsiku la anakubala kudzera mu pologalamu ya Zokonda Amayi wu mawa lino.
A Senga, omwenso ndiogwilizira udindo wa mkulu oyang’anira nkhani ku MBC, adatinso ndipofunika kuti amayi akhale ndimaphunziro osiyanasiyana monga a zamalonda ndi zaumoyo.
Olemba: Chisomo Manda