Pamene dziko la Malawi likuyembekezera gawo lachiwiri la ndalama za mungongole yotchedwa Extended Credit Facility kuchokera ku bungwe la IMF, unduna wa zachuma wati ngakhale ndondomeko zachuma zomwe zinapangitsa kuti IMF iyambenso kupereka ngongoleyi zakumana ndimavuto, ndondomekozi zili m’chimake.
Nduna ya zachuma, a Simplex Chithyola Banda ati mwachitsanzo, mayiko ndi mabungwe ena avomereza ku khonzanso ngongole za dziko lino, boma likugwiritsa ntchito ndalama mosamala, ndalama zakunja zikupezeka m’dziko muno, alemba ntchito mkulu watsopano ku bungwe lotolera misonkho la MRA kuti bungweli lizitolera ndalama zokwanira komanso akusintha malamulo ena azachuma.
A Chithyola Banda ati ndi chikhulupiliro kuti IMF ikhutitsidwa ndi m’mene chuma chikuyendera ndipo ipereka gawo lachiwiri la ngongoleyi.