Mtsogoleri wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Thom Mpinganjira wapepesa otsatira timu yi chifukwa chogonja ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets dzulo loweluka ndizigoli ziwiri kwa chimodzi.
Kudzera mu chikalata chomwe watulutsa, Mpinganjira wayamikira manoma onse kaamba kosunga mwambo atangonja, ndipo akuti timuyi ichitapo kanthu kuti zinthu zisinthe.
Iye wati wawerenga ndi kumva madandaulo komanso nkhawa zonse zomwe otsatirawa apereka kudzera mu masamba amchezo ndipo walonjeza kuti azigwiritsa ntchito pofuna kukonza mavuto ku Wanderers.
Kugonjaku kwadzetsa nkhawa pa tsogolo lawo lolimbirana ukatswiri wa mpikisano wa TNM ndi timu ya Silver Strikers.
Olemba : Amin Mussa