Mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Lazarus Chakwera, masana ano akuyembekezeka kucheza ndi ochita malonda ochokera mmisika yosiyanasiyana ya kuchigawo chakummawa kwa dziko lino.
Ochita malonda osachepera 300 ndiwo afika kunyumba ya boma ya Chikoko Bay ku Mangochi.
Mwazina, Dr. Chakwera akufuna kumva ena mwa mavuto amene anthuwa akukumana nawo komanso kupeza ena mwa mayankho a mavutowo.
Ena mwa ochita malondawa achokera ku misika ya ku Zomba, Machinga-Ntaja, Nsanama, Liwonde, Mangochi ndi misika ina.
Olemba: Mirriam Kaliza