Sitima yochekera ku Beira m’dziko la Mozambique itha kufika ku Marka m’boma la Nsanje, atero a Chithyola Banda.
Nduna ya zachuma yi yatsindika kuti ntchito yokonza njanji ya sitima kuchoka ku Marka kufika ku Bangula yafika pamapeto, ndipo sitima itha kufika kuchoka ku Beira.
Iwo ayi izi zithandiza kupititsa chuma cha dziko lino patsogolo, maka kupyolera mu ntchito za malonda.