M’modzi mwa oyimba nyimbo zauzimu m’dziko muno, Ethel Kamwendo, walangiza oyimba nyimbo zauzimu kuti asakomedwe ndi ndalama koma agwiritse maitanidwe awo pomaimba nyimbo zolimbikitsa miyoyo ya anthu omwe akusautsika ndi mikwingwilima yodza kaamba ka uchimo.
Kamwendo wati chaka cha 2024 anakhuzidwa kwambiri ati poti panali kusakanikilana kwambiri pakati pa oyimba zauzimu ndi oyimba zachikunja zomwe wati zikuika pachiopyezo kuti zitha kusungunula cholinga chenicheni cha maitanidwe.
“Sizoona kuti oyimba nyimbo zauzimu tidzingoti uku talowera uku talowera. Tidziwe kuti tili ndi maitanidwe omwe titha kuphonya pa cholinga cha Mulungu ngati sitisamala,” anatero Kamwendo.
Kamwendo watinso chaka cha 2025 iye akhala akupitiriza kuimba nyimbo zobukitsa dzina la Yesu. Iye walangizanso achinyamata kuti adzizisamala popewa mchitidwe wachisawawa monga uhule, mowa komanso kusuta kuti miyoyo yawo ikhale yaitali.