Ntemi Gwabatemi Kyungu yamaboma a Chitipa ndi Karonga yapempha ogwira ntchito muzipatala za m’dziko muno kukhala odzipereka pothandiza odwala komanso ndikukonda dziko lawo.
Mfumuyi yanena izi pomwe iyo ndi mafumu andodo aboma la Karonga anakwwona ndi kucheza ndi odwala pachipatala cha Karonga pokondwelera chaka chatsopano.
Mkulu woona zaumoyo ndi ukhondo m’boma la Karonga, a David Sibale, anayamikira mfumuyi kaamba kopereka thandizoli lomwe anati labwera panthawi yake.
Pamwambowu panalinso Ntemi Kalonga, Ntemi Mwakaboko, Ntemi Mwangolera, Ntemi Mwinuka ndi amai akunyumba zachifumuzi.
Odwala omwe anawayenda ndi akuchipinda cha amuna ndipo analandira maphukusi akatundu monga sopo wochapila, wosambila, buledi ndi zakumwa za frooty.