Zokonzekera zonse za phwando la mayimbidwe limene likutchedwa kuti Nde’feyo legacy, lomwe lichitikire ku 24/7 ku Blantyre lero, zili mchimake.
Mwambowu ubweretsa pamodzi oyimba asanu amene anasayinidwa ndi kampani ya Nde’feyo pomwe ankayamba kuyimba monga Maskal, Piksy, Onesimus, Trumel ndi Bucci.
Poyankhula ndi MBC, mmodzi wa oyimba-wa, Maskal, yemwe wabwera m’dziko muno kuchokera ku America komwe amakhala, wati anthu akonzekere mayimbidwe apamwamba.
Wolemba: Simeon Boyce