Prezidenti Dr Lazarus Chakwera wauza anthu amchigawo chakumpoto kuti boma lake ladzipereka potukula miyoyo ya anthu mdziko muno kudzanso mchigawochi.
Dr Chakwera amalankhula pa Katoto mu mzinda wa Mzuzu pofika mchigawochi komwe khwimbi linasonkhana pomulandira.
Mtsogoleriyu wapemphanso anthu mdziko muno kuti alimbikitse umodzi.