Madotolo okwana khumi (10) ochokera m’dziko la America, omwe ndi akatswiri azachipatala pokonza nkhope za anthu, afika m’dziko muno kudzagwira ntchitoyi.
Malinga ndi yemwe watsogolera gulu lama dotololi, Dr Tania Nkungula, ntchitoyi, yomwe ikhale yamasabata awiri, ayigwira pachipatala cha Queen Elizabeth Central Hospital mu mzinda wa Blantyre.
” Ambiri mwa anthu [odwala] amakhala kuti mwazina ali ndi zotupa mkamwa komanso ovulala nkhope pa ngozi zosiyanasiyana,” atero Dr Nkungula.
Poyankhula atalandira alendowa pa bwalo la ndege la Chileka ku Blantyre, kazambe wadziko lino ku America, a Esme Chombo, ati madotolo wa athandiza anthu pafupifupi 40 omwe ali ndi mavuto otere.
Dziko lino lili ndi dotolo m’modzi yekha odziwa za ukadaulo otere.